
Masomphenya athu
Timakhulupilira mu kuthekera kwa anthu. ZikomoFoundation imakhulupilira kutukula anthu, pakutukula anthu muwathandiza kuti athane ndi masautso awo.
Cholinga yathu
Chilinga chathu chachikulu ndi kupititsa patsogolo kuthekera kwa ana. Kuonetsetsa kuti ana ali ndi chiyembekezo ndi tsogolo.
Kumene tikugwira ntchito
Pakali pano ntchito yathu ili ku Malawi, makamaka chigawo chapakati ku Lilongwe


Mbiri yathu

Gulu lathu
Maziko athu
-
Ogwira ntchito
-
« Ndikadzuka tsiku lililonse, ndimakhala okondwa kuti ife sitimangoganiza zochita zinthu zolondola koma kuti timachita zinthu zolondola »
Simon Holdener Oyambitsa bungwe
-
«Ndine okondwa kugwira ntchito ndi Zikomo Foundation. Masomphenya ake kuthandiza ana ndiogwira mtima. Ndili ndikufunitsitsa kuthandiza Africa, ndipo kugwira ntchito ndi ana ndiye tsogolo la Africa. »
James Phiri Wotsogolera ku Malawi
-
« Ndikuthandiza ntchito za Zikomo Foundation chifukwa ndimakhulupilira chitukuko cha mbali zonse. kungogawa zinthu zimakhala thandizo la lero lokha koma kusintha kaganizidwe ndi machitidwe komanso maphunziro ndi zinthu zokhazikika.»
Jürg Opprecht (†) wazamalonda
-
« Lero timakonda kukamba za vuto la kuchuluka kwa anthu othawa nkhondo ku maiko akwawo. Anthu mazanamaza a ku Africa amabwera kwathu kuno chifukwa cha mavuto amene ali m'dziko mwao. Kuti alimbikitsike ndi kusintha miyoyo yawo kuti akhoza kuchitapo kanthu za za m'maiko awo akufunika mabungwe ngati Zikomo Foundation.»
Marc Jost Khansala wa mzinda wa Bern
-
« Ndikukumbukira bwino kuti umoyo ndi khalidwe langa lidakonzeka chifukwa cha masewero a mpira. Ndaphunzira khalidwe labwino, kupilira ndikulimbana ndi kulephera. Ndiliokondwa ndi ntchito komanso njira zimene Zikomo Foundation ikutsata ndipo ndimakondwa kuthandiza ntchito zimenezi. »
Roman Josi Osewera Hoke NHL ochokera ku dziko lina
-
«Ine ndidabadwira ndi kukulira ku Africa. Ndikudziwa bwino m'mene masewera ampira amasinthira miyoyo. Kudzera mumasewero a mpira ndaphunzira kulimbikira ndikukwaniritsa zinthu zosiyanasiyana. Ndimtima wanga onse ndikuthandiza ntchito za Zikomo Foundation. »
Gilles Yapi Osewera Mpira kunja kwa dziko lake
-
« Kutukula anthu zikutanthauza kuwapatsa tsogolo ndi chiyembekezo »
Simon Holdener Oyambitsa bungwe
-
« Ndimadziwana bwino ndi otsogolera bungwe la Zikomo Foundation Simon Holdener. Bungweli likugwira ntchito yotamandika kwambiri yomwe ikubweretsa kusintha kosiyanasiyana m'miyoyo ya anthu aku Malawi. Ndikudziwa kuti ndili ndi udindo othandiza, nchifukwa chake ndikuthandiza bungweli.»
Mark Streit Osewera wakale wa hoke NHL
-
«Ndimathandiza Zikomo Foundation chifukwa kupyolera mu ntchito zawo ndikufikira anthu ochuluka. Pakuphunzitsa aphunzitsi, nde kuti ananso aphunzitsidwa bwino ndipo miyoyo yawo isintha kwakukulu »
Andreas Thür Wojambula zomangamanga
-
« Ndidali ndi mwayo okonza nawo mgonero wa Zikomo Foundation. Ndikhoza kufotokoza kuti ogwira ntchito olembedwa ndi ongodzipereka akugwira ntchito molimbika ndi kukhudzika konse ku Malawi. Ndikukhulupilira kuti Zikomo Foundation ipereka mwai ndikuthandiza kwakukula ana m'dziko la Malawi. "
Lukas Ninck Wogwira ntchito ku wailesi ya kanema
-
" Ndimasangalala kugwira ntchito ndi Zikomo Foundation chifukwa cha masomphenya ake. Ana ndi achinyamata ku Malawi apeza kuthekera kofikira ndi kupeza maphunziro apamwamba komanso kuphunzira luso la masewero a mpira la pamwamba. Zikomo Foundation ikupereka ndikugwira ntchito zapamwamba kwambiri. »
Davie Mpima Mkulu oyang'anira ndikuyendetsa masewero amphira ku Malawi