






Ndife bungwe la chitukuko lomwe likulu lake lili ku Switzerland ndi ofesi ina ku Malawi. Pakadali pano tikugwira ntchito zathu ku Malawi ndipo tikufunitsitsa kuti anthu okwana 100’000 afikiridwa, ndipo kuti pofika 2020 anthu afikilidwa m’madera atatu awa:

Maphunziro
Mwana aliyense ali ndi ufulu wa maphunziro
Kudzera ku ma phunziro kuthekera kwanu konse kumatulukira.


Ntchito
Timakhulupilira kuthekera kwa munthu
Timalenga ntchito zomwe tikupereka mwayi ochuluka kwa anthu
«Kuyambira chaka cha 2012 takhala tikugwira ntchito ndikuonetsetsa kuti ana 100’000 aku Malawi ali ndi mwayi wa maphunziro, moyo wathanzi, ndi zamasewero. Ana a ku Malawi akhale ndi chiyembekezo ndikutenga tsogolo lawo m’manja mwao.»
– Simon Holdener, Oyambitsa bungwe


Kodi mukudziwa...
...kuti zaka zokhala ndi moyo zili cha m'ma 45?
Kodi mukudziwa...
...kuti ana 9 okha pa 100 alionse ku Malawi ali ndi mwayi wa maphunziro a mkomba phala?
Kodi mukudziwa...
...ku Malawi mkalasi imodzi mumatha kukhala ana 76
Kodi Mukudziwa...
...kuti Malawi ndi limodzi mwa maiko 5 osauka?
Kodi mukudziwa...
...kuti ku Malawi anthu 0.35 mwa 100 adachita maphunziro a ukachenjede?